Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 83

“Kunyumba ndi Nyumba”

Sankhani Zoti Mumvetsere
“Kunyumba ndi Nyumba”
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Machitidwe 20:20)

 1. 1. Kunyumba ndi nyumba

  Ife timalalikira.

  Kulikonse nkhosa za M’lungu,

  Zikudyetsedwa.

  Zoti Ufumu wa M’lungu

  Ukulamulira,

  Akhristu, tikulengeza

  Akulu ndi ana.

 2. 2. Khomo ndi khomo,

  Tinene za chipulumutso.

  Dzina la M’lungu aitane

  Apulumuke.

  Adzaitana bwanji

  Dzina lomwe sadziwa?

  Choncho kumakomo awo

  Tidzalilengeza.

 3. 3. Khomo ndi khomo

  Tiyeni tifalitse mawu.

  Asankhe okha kumvera,

  Kapena kukana.

  Koma dzina la Yehova

  Tidzalengezabe.

  Ndipo potero,

  Tidzapezadi nkhosa zake.