Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

MITU YA NKHANI

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 82

“Onetsani Kuwala Kwanu”

Sankhani Zoti Mumvetsere
“Onetsani Kuwala Kwanu”
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 5:16)

 1. 1. Yesu walamula

  Kuti tiwale,

  Monga dzuwa

  Limawalira onse.

  Mawu a mtendere,

  Ali m’Malemba.

  Choncho tizisonyeza

  Kuwala kwa Ya.

 2. 2. Uthenga wa M’lungu

  Onse amvetu,

  Uzitiwalira

  Polalikira.

  Mfundo za cho’nadi

  Zitsogolere.

  Anthu asankhe okha,

  Kumva uthenga.

 3. 3. Tikamasonyeza

  Kukoma mtima,

  Timawalitsadi

  Dziko la mdima.

  Choncho tisonyeze

  Kuwala kwathu,

  Tikatero Mulungu

  Asangalala.