ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mlaliki 11:6)

 1. 1. M’mawa uliwonse, tulo tisanathe,

  Timadzuka n’kupita

  kolalikira uthenga.

  Ndipo Mulungu amatitsogolera

  Timakondwa anthu

  akamamvetsera uthenga.

  (KOLASI)

  Tinasankha,

  kutumikira Yehova.

  Timachita zofuna zake.

  Tipitirizabe kulalikiraku,

  Tikatero timasonyeza

  Chikondi.

 2. 2. Pofika madzulo, timatopa ndithu,

  Komabe timapeza

  chimwemwe potumikira.

  Madalitso Yehova amatipatsa

  Nthawi zonse

  timamuthokoza potithandiza.

  (KOLASI)

  Tinasankha,

  kutumikira Yehova.

  Timachita zofuna zake.

  Tipitirizabe kulalikiraku,

  Tikatero timasonyeza

  Chikondi.