Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 8

Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu
ONANI

(Salimo 91)

 1. 1. Yehova m’pothawira,

  Timamudalira.

  Tikhalebe mumthunzi;

  Wake tisachoke.

  Iye adzatiteteza,

  Tikhulupirire ndithu.

  Yehova mphamvu zathu,

  Ateteza olungama.

 2. 2. Kaya ambiri agwe

  Pafupi ndi ife,

  Yehova satisiya

  Adzatiteteza.

  Choncho tisachite mantha;

  Tsoka silidzatigwera.

  Yehova M’lungu wathu,

  Adzatibisa m’mapiko.

 3. 3. Ku misampha yambiri

  Adzatiteteza,

  Zoopsa zilizonse,

  Sitidzaziopa.

  Zoopsa zonse zidzatha

  Kulikonse tidzapita.

  Yehova m’pothawira,

  Adzatiteteza ndithu.