ONANI

(Machitidwe 18:11)

 1. 1. Ophunzitsa choonadi,

  Amasangalala.

  Timapeza madalitso

  Ochuluka ndithu.

  Timatsanziratu Yesu

  Pophunzitsa ena.

  Ndipo timawathandizatu

  Kukonda Mulungu.

 2. 2. Pamene tikuphunzitsa,

  Tichite zabwino,

  Anthu onse aonetu

  Kuwala kwa M’lungu.

  Timafufuza mwakhama,

  Mawu a Mulungu.

  Pouza ena uthengawu

  Timaphunziranso.

 3. 3. Zofunika pophunzitsa

  M’lungu watipatsa.

  Ndipo tikamamupempha,

  Adzatithandiza.

  Timakonda Mawu ake;

  Omwe ndi oona.

  Tikakonda ophunzira,

  Adzatumikiranso.