ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Aheberi 13:15)

 1. 1. Kodi m’mamva bwanji

  m’kazindikira kuti,

  mwasonyezadi khama

  pophunzitsa ena?

  Inde m’kayesetsa,

  M’lungu adzadalitsa.

  Mudzathandiza anthu

  kudziwa Mulungu.

  (KOLASI)

  Timasangalala ndithu

  kupereka mtima wathu.

  Choncho tim’tumikirebe

  tsiku lililonse.

 2. 2. Kodi m’mamva bwanji

  m’kazindikira kuti,

  mwawafika pamtima

  akamva uthenga?

  Ena amakana,

  ena kunamizidwa.

  Koma timanyadira

  tikalalikira.

  (KOLASI)

  Timasangalala ndithu

  kupereka mtima wathu.

  Choncho tim’tumikirebe

  tsiku lililonse.

 3.  3. Kodi m’mamva bwanji

  m’kakumbukira kuti,

  mwa chikondi Yehova

  amatsogolera?

  Timalalikira,

  anthu timaphunzitsa,

  akhale ndi tsogolo

  adzapeze moyo.

  (KOLASI)

  Timasangalala ndithu

  kupereka mtima wathu.

  Choncho tim’tumikirebe

  tsiku lililonse.