ONANI

(Salimo 98:1)

 1. 1. Iyi ndi nyimbo yachisangalalo;

  Yolemekeza M’lungu wamkulu.

  Imatipatsadi chiyembekezo.

  Imbani nafe nyimbo yathuyi:

  (KOLASI)

  ‘Lambirani M’lungu wathu,

  Mwana waketu ndi Mfumu!

  Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu

  Tamandani dzina la Mulungu.’

 2. 2. Ndi nyimboyi tilengeza Ufumu.

  Khristu Yesu ndi wolamulira.

  Ndipo mtundu watsopano wabadwa

  Nawo ukumusangalalira.

  (KOLASI)

  ‘Lambirani M’lungu wathu,

  Mwana waketu ndi Mfumu!

  Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu

  Tamandani dzina la Mulungu.’

 3. 3. Nyimboyi omwe angaiphunzire,

  Ndi amene amadzichepetsa.

  M’dziko lonse ambiri aphunzira.

  Akuitananso anthu ena.

  (KOLASI)

  ‘Lambirani M’lungu wathu,

  Mwana waketu ndi Mfumu!

  Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu

  Tamandani dzina la Mulungu.’