ONANI

(Machitidwe 4:29)

 1. 1. Polalikira Ufumu,

  Kukweza dzina lanu,

  Anthu ena amatsutsa,

  Ndiponso kutinyoza.

  Koma sitiwaopa,

  Timamvera inu nokha.

  Choncho Yehova, tikupempha;

  Mutipatse mzimu wanu.

  (KOLASI)

  Polalikira uthenga,

  Mutichotsere mantha.

  Tikhale olimba mtima

  Anthu amve uthenga.

  Amagedo ikufika,

  Tikhale olimba mtima,

  Tithandizeni Yehova.

  Tikupempha.

 2.  2. Pamene tichita mantha,

  Mudziwa ndife fumbi.

  Mudzatithandiza ndithu

  Paja munalonjeza.

  Imvani kuopseza,

  Kwa anthu odana nafe.

  Tithandizeni, tisaope

  Tikhale olimba mtima.

  (KOLASI)

  Polalikira uthenga,

  Mutichotsere mantha.

  Tikhale olimba mtima

  Anthu amve uthenga.

  Amagedo ikufika,

  Tikhale olimba mtima,

  Tithandizeni Yehova.

  Tikupempha.