Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 70

Fufuzani Anthu Oyenerera

Sankhani Zoti Mumvetsere
Fufuzani Anthu Oyenerera
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 10:11-15)

 1. 1. Ambuye wathu anatisonyeza,

  Njira yolalikirira:

  ‘Fufuzani anthu oyenerera,

  Ofuna kumva choonadi.

  Muziwapatsa moni eni nyumba,

  Ndi kuwafunira mtendere.

  Ngati sanakulandireni,

  Sasani fumbi m’mapazi muchoke.’

 2. 2. Onse amene akulandirani,

  Alandiranso Ambuye.

  Athandizeni kusonyeza mtima

  Wofuna kudziwa cho’nadi.

  Musadere nkhawa zoti munene,

  Yehova akuthandizani.

  Mawu anu akakhala okoma

  Ofatsa adzasangalala.