Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

MITU YA NKHANI

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 68

Tizifesa Mbewu za Ufumu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Tizifesa Mbewu za Ufumu
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 13:4-8)

 1. 1. Bwerani mudzagwire ntchito;

  Yotumikira Ambuye.

  Iye adzakuthandizani;

  Mukamvera malangizo.

  Mbewu za cho’nadi zidzakula

  M’mitima ya omvetsera.

  Choncho tumikirani mwakhama

  Pa ntchito imene mwapatsidwa.

 2. 2. Kuti ntchito iyende bwino

  Zingadalire inuyo.

  Mukaphunzitsa bwino anthu

  Adzakondatu cho’nadi.

  Muwathandizetu kupirira

  Mavuto apadzikoli.

  Mudzasangalalatu kuona

  Akukonda cho’nadi kwambiri.