Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 65

Pita Patsogolo

Sankhani Zoti Mumvetsere
Pita Patsogolo
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Aheberi 6:1)

 1. 1. Pita patsogolo khala wolimba!

  Onetsa kuwala anthu onse aone.

  Sonyezatu luso muutumiki;

  M’lungu adzathandiza.

  Utumikiwu ndi wa onse.

  Yesu naye anauchita.

  Dalira Mulungu kuti usagwe,

  Gwiritsa chilungamo.

 2. 2. Pita patsogolo molimba mtima!

  Uzilalikira ku mtundu uliwonse.

  Tamanda Yehova Mfumu yathuyo,

  Polalikira nawo.

  Adani angatiopseze,

  Tisaleke, onse amvetu.

  Kuti Ufumu wa M’lungu wayamba.

  Phunzitsa choonadi.

 3.  3. Pita patsogolo usabwerere,

  Wonjezera luso

  ntchito ndiyaikulu.

  Mzimu wa Mulungu ukuthandize,

  Udzapeza chimwemwe.

  Konda anthu omwe wapeza.

  Bwerera, uwafike m’mtima.

  Athandize apite patsogolo,

  Cho’nadi chiziwala.