Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 63

Ndife Mboni za Yehova

Sankhani Zoti Mumvetsere
Ndife Mboni za Yehova
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Yesaya 43:10-12)

 1. 1. Apanga timilungu,

  M’lungu wo’na sam’dziwa.

  Ndi Wamphamvuyonse,

  Monga tidziwa.

  Milunguyo sidziwa,

  Zomwe zili mtsogolo.

  Milunguyo ilibe mboni,

  Chifukwatu ndi yabodza.

  (KOLASI)

  Mboni za Yehovafe.

  Tinena mosaopa.

  M’lungu wathu akalosera;

  Ndithu zimachitika.

 2. 2. Timalengeza dzina

  La Yehova Mulungu.

  Ndi Ufumu wake,

  Molimba mtima.

  Timathandiza ena,

  Kudziwa choonadi.

  Akamalimba adzaimba,

  Nyimbo yotamanda M’lungu.

  (KOLASI)

  Mboni za Yehovafe.

  Tinena mosaopa.

  M’lungu wathu akalosera;

  Ndithu zimachitika.

 3.  3. Ntchito yolalikira,

  Za dzina la Yehova.

  Imachenjezadi,

  Olidetsawo.

  Imathandiza anthu,

  Kukhululukidwadi.

  Imabweretsanso chimwemwe,

  Komanso chiyembekezo.

  (KOLASI)

  Mboni za Yehovafe.

  Tinena mosaopa.

  M’lungu wathu akalosera;

  Ndithu zimachitika.