Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 62

Nyimbo Yatsopano

Sankhani Zoti Mumvetsere
Nyimbo Yatsopano
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 98)

 1. 1. Imbira M’lungu, Imba nyimbo yatsopano.

  Unene kwa onse Ntchito zake zonse.

  Umutamande, Mulungu ndi wopambana.

  Poweruza anthu

  Ndi wachilungamo.

  (KOLASI)

  Imbani!

  Nyimbo yatsopano.

  Imbani!

  Yehova ndi Mfumu.

 2. 2. Fu’la mokondwa, Fuula kwa Mfumu yathu!

  Mutamandenitu, Ndi nyimbo mokondwa.

  Tiyeni tonse Timuimbire mokweza.

  Zeze ndi lipenga

  Ziimbe pamodzi.

  (KOLASI)

  Imbani!

  Nyimbo yatsopano.

  Imbani!

  Yehova ndi Mfumu.

 3. 3. Nyanja ndi zinthu Za mmenemo zim’tamande.

  Inde zolengedwa, Zonse zim’tamande.

  Mtunda ukondwe, Mitsinjenso ikondwere.

  Mapiri ndi zigwa,

  Nazo zim’tamande.

  (KOLASI)

  Imbani!

  Nyimbo yatsopano.

  Imbani!

  Yehova ndi Mfumu.