Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

MITU YA NKHANI

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 61

Pitani Patsogolo Mboninu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Pitani Patsogolo Mboninu
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Luka 16:16)

 1. 1. Olimba m’nthawi yamapeto ino,

  Ndi atumiki oteteza uthenga.

  Mdyerekezi amawatsutsa.

  Mumphamvu ya Yehova samagonja.

  (KOLASI)

  Ndiye pitani patsogolo Mboninu!

  Kondwerani pogwira ntchito ya M’lungu!

  Uzani onse zadziko latsopano

  Mmene mudzakhala madalitso.

 2. 2. Tisatengeke ndi moyo wofewa,

  Kusangalatsa dzikoli tizipewa.

  Mawanga a dziko tikane

  Ndi kukhala okhulupirikabe.

  (KOLASI)

  Ndiye pitani patsogolo Mboninu!

  Kondwerani pogwira ntchito ya M’lungu!

  Uzani onse zadziko latsopano

  Mmene mudzakhala madalitso.

 3. 3. Ufumu wa M’lungu ukunyozedwa,

  Dzina lake loyera likudetsedwa.

  Tiyenitu tiliyeretse,

  Kumitundu yonse tililengeze.

  (KOLASI)

  Ndiye pitani patsogolo Mboninu!

  Kondwerani pogwira ntchito ya M’lungu!

  Uzani onse zadziko latsopano

  Mmene mudzakhala madalitso.