ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 19)

 1. 1. Kumwamba kumatamanda Yehova.

  Ntchito zake zonse

  ndi zoonekera.

  Tsiku ndi tsiku zimam’tamanda.

  Nyenyezi zimasonyeza

  kuti ndi wamphamvu.

 2. 2. Malamulo a M’lungu ndi angwiro,

  Mawu ake onse

  amatiteteza.

  Amaweruzanso molungama.

  Mawu ake ndi oona,

  N’ngoyera, n’ngokoma.

 3. 3. Tidzaopa Mulungu kwamuyaya.

  Malamulo ake

  aposa golide.

  Iwotu amatitsogolera.

  Dzina lake loyeralo

  Tililemekeze.