Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 59

Tamandani Ya Limodzi ndi Ine

Sankhani Zoti Mumvetsere
Tamandani Ya Limodzi ndi Ine
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 146:2)

 1. 1. Titamande;

  Ya mokweza!

  Amatipatsa zonse zabwino.

  Tsiku lonse,

  Tim’tamande,

  Ndi wachikondi, n’ngwamphamvu zonse.

  Ndipo dzina lake tilengeze.

 2. 2. Titamande;

  Ya chifukwa.

  Amatimva tikamapemphera.

  Dzanja lake

  Ndi lamphamvu;

  Amalimbikitsa ofooka.

  Za mphamvu zake timalengeza.

 3. 3. Titamande;

  Ya mokondwa.

  N’ngolungama ndi wodalirika.

  Adzakonza

  Zolakwika.

  Ndipo anthu adzadalitsidwa.

  Timutamande mosangalala!