Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 55

Musawaope!

Sankhani Zoti Mumvetsere
Musawaope!
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 10:28)

 1. 1. Pitanibe anthu anga,

  Lengezani Ufumu.

  Musaope mdaniyo.

  Dziwitsani achidwi

  Kuti Mwana wanga Yesu,

  Wagwetsadi mdaniyo,

  Posachedwa adzam’manga,

  Sadzazunzanso anthu.

  (KOLASI)

  Musaope anthu anga,

  Kaya akuopseni.

  Ndidzakutetezerani

  Monga mwana wa diso.

 2. 2. Adani angachuluke,

  Ndi kukuopsezani,

  N’kukunyengererani,

  Kuti mupusitsidwe.

  Musaope anthu anga,

  Kaya akuzunzeni,

  Ndidzakutetezerani

  Mpaka onse atatha.

  (KOLASI)

  Musaope anthu anga,

  Kaya akuopseni.

  Ndidzakutetezerani

  Monga mwana wa diso.

 3.  3. Sindingakuiwaleni,

  Ndidzakutetezani.

  Ngakhale akupheni,

  Ndidzagonjetsa imfa.

  Musaope opha thupi

  Sangawononge moyo.

  Choncho khulupirikani;

  Mudzalandira moyo.

  (KOLASI)

  Musaope anthu anga,

  Kaya akuopseni.

  Ndidzakutetezerani

  Monga mwana wa diso.