Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 48

Tiziyenda ndi Yehova Tsiku Lililonse

Sankhani Zoti Mumvetsere
Tiziyenda ndi Yehova Tsiku Lililonse
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mika 6:8)

 1. 1. Timayenda ndi Atate,

  Nthawi zonse modzichepetsa.

  N’ngokoma mtima kwa anthu

  Ochita zomusangalatsa.

  Ndipo anakonza njira,

  Kuti tiyende naye.

  Choncho tidzipereketu,

  Potumikira Yehova.

 2. 2. Mapeto ali pafupi,

  Ndipo Satana ndi wokwiya.

  Timatsutsidwa kwambiri,

  Choncho tingamachite mantha.

  Yehova atiteteza,

  Tikamuyandikira.

  Tim’tumikire kosatha,

  Tim’konde ndi mtima wonse.

 3. 3. M’lungu akutithandiza,

  Ndi mzimu ndi Mawu akenso.

  Kudzera mu mpingo wake,

  Amamvanso pemphero lathu.

  Tikayenda ndi Yehova,

  Tidzachita zabwino.

  Choncho tikhulupirike,

  N’kukhala odzichepetsa.