Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 47

Muzipemphera kwa Yehova Tsiku Lililonse

Sankhani Zoti Mumvetsere
Muzipemphera kwa Yehova Tsiku Lililonse
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(1 Atesalonika 5:17)

 1. 1. Pemphera kwa Yehova amamva.

  Ndi mwayi umene watipatsa.

  Umuuze zamumtima mwako,

  Ndi wodalirika, bwenzi lako.

  Pempherabe kwa M’lungu.

 2. 2. Pemphera kwa M’lungu uthokoze.

  Tim’pemphe atikhululukire.

  Timuuze zomwe talakwitsa,

  Amadziwa zofooka zathu.

  Pempherabe kwa M’lungu.

 3. 3. Pemphera kwa M’lungu zikavuta,

  Ndi Tate wathu amathandiza.

  Um’pemphe kuti akuteteze,

  Um’khulupirire usaope.

  Pempherabe kwa M’lungu.