Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

MITU YA NKHANI

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 46

Timakuyamikirani Yehova

Sankhani Zoti Mumvetsere
Timakuyamikirani Yehova
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(1 Atesalonika 5:18)

 1. 1. Tikuyamikani Yehova M’lungu,

  Mumatipatsa kuwala kwanu.

  Tikuyamika mwayi wa pemphero,

  Kuti tinene mavuto athu.

 2. 2. Tikuyamika potumiza Yesu,

  Amene anagonjetsa dziko.

  Tikuyamikani potithandiza

  Kukwaniritsa lonjezo lathu.

 3. 3. Tikuyamika chifukwa cha mwayi

  Wolalikira za dzina lanu.

  Tiyamika mudzathetsa mavuto,

  Madalitso anu sadzathadi.