ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 19:14)

 1. 1. Zomwe ndimasinkhasinkha,

  Zimene ndimaganiza​—

  Zikusangalatseni Ya,

  Kuti ndikhale wolimba.

  Pamene ndili ndi nkhawa

  N’kumalephera kugona,

  Ndisinkhesinkhe za inu

  Inde zinthu zoyenera.

 2. 2. Zilizonse zolungama,

  Zofunika ndi zoona,

  Ndikamaziganizira​—

  Zindipezetse mtendere.

  Nzeru zanu n’zofunika

  Komanso ndi zochuluka.

  Choncho ndizisinkhasinkha

  Zonena zanu mwakhama.