Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

MITU YA NKHANI

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 43

Pemphero Loyamikira Mulungu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Pemphero Loyamikira Mulungu
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 95:2)

 1. 1. Yehova tikukuyamikirani.

  Kudzera mupemphero lathuli.

  Mofunitsitsa tidzatumikira,

  Timadziwa mumatithandiza.

  Nthawi zina timakuchimwirani.

  Tipempha mutikhululukire.

  Tikuthokoza munatiwombola.

  Mumadziwanso ndife ofo’ka.

 2. 2. Tikuyamika mumatikondatu.

  Munatikokeranso kwa inu.

  Mutidziwitse za inu Mulungu

  Mutiphunzitse kukukondani.

  Mzimu wanu umatithandizadi.

  Timalankhula molimba mtima.

  Titumikire modzichepetsadi;

  Timakuthokozani Yehova.