ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Aefeso 6:18)

 1. 1. M’lungu, Atate, Wamphamvuyonse,

  Dzina lanulo liyeretsedwetu.

  Mumachita zomwe mwafuna,

  Tikupempha Ufumu ubwere.

  Pa nthawi yanu M’lungu,

  Tidzadalitsidwetu.

 2. 2. Mumatichitiranso zabwino,

  Mphatso zoti sitikanazipeza.

  Ndinu Gwerodi la kuwala,

  Mwatithandiza kupeza nzeru.

  Tizikuthokozani,

  Chifukwa cha chikondi.

 3. 3. Zotisautsa m’dziko n’zambiri

  Tikupempha muzititonthozadi.

  Nkhawa zathu tipatsa inu,

  Muzitithandiza kupirira.

  Malonjezo athunso,

  Tiwakwanitse ndithu.