NYIMBO 40
Kodi Ndife a Ndani?
Sankhani Zoti Mumvetsere
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi
1. Iwe ndi wandani?
Umvera m’lungu uti?
Amene umam’gwadirayo.
Iye ndiye m’lungu wako.
Milungu iwiri;
Sungaitumikire.
Sungalambire iwiri yonse,
Sankhapo mmodzi yekha.
2. Iwe ndi wandani?
Umvera m’lungu uti?
Zilitu ndi iwe kusankha,
Woona kaya wonama.
Kodi Kaisara
Udakamukondabe?
Kapena udzamvera Yehova
N’kugwira ntchito yake?
3. Ine ndi wandani?
Ndidzamvera Yehova.
Atate wanga wakumwamba;
Ine ndidzam’sangalatsa.
Anandigulatu;
Ndidzamutumikira.
Ndizim’lambira, dzina lakenso
Ndizililemekeza.
(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 116:14, 18; 2 Tim. 2:19.)