ONANI

(Mlaliki 7:1)

 1. 1. Pamoyo wathu, Tsiku lililonse

  Tipange dzina Labwino ndi M’lungu.

  Tikachita zinthu Zabwino kwa M’lungu,

  Tisangalatsa Mtima wake.

 2. 2. Kufunitsitsa Kutchuka m’dzikoli,

  N’cholinga choti Anthu atikonde.

  Kulibetu phindu Chifukwa Yehova,

  Sangatikonde Tikatero.

 3. 3. Tifuna M’lungu Atilembe dzina

  Kuti tikhale, Mu buku la moyo.

  Choncho tikhaletu Ndi dzina labwino

  Kwa M’lungu wathu, Nthawi zonse.