Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 37

Kutumikira Yehova ndi Moyo Wathu Wonse

Sankhani Zoti Mumvetsere
Kutumikira Yehova ndi Moyo Wathu Wonse
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 22:37)

 1. 1. Yehova Wamphamvuyonse,

  Inetu ndimakukondani.

  Mtima wanga wonse umafuna;

  Kukutumikirani.

  Malamulo anu ndimvera,

  Zofuna zanu ndichita.

  (KOLASI)

  Inu Yehova ndinu woyenera

  Kutumikiridwa.

 2. 2. Atate zomwe munalenga

  Zimakulemekezani.

  Ndi mphamvu zangatu zonse,

  Ndidzauza ena za inu.

  Ndithandizenitu Yehova,

  Kuti ndikhulupirike.

  (KOLASI)

  Inu Yehova ndinu woyenera

  Kutumikiridwa.