ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Miyambo 4:23)

 1. 1. Titeteze mtima wathu;

  Tikhale ndi moyo.

  M’lungu amadziwa bwino

  Za mumtima mwathu.

  Mtima ndi wonyenga,

  Ungatisocheretsetu.

  Choncho tiganize bwino

  Timvere Yehova.

 2. 2. Timafunafuna M’lungu

  Tikamapemphera.

  Timathokozadi zonse,

  Zomwe amachita.

  Zimene amaphunzitsa

  Timazitsatira.

  Ndipo tikhulupirike

  Timusangalatse.

 3. 3. Titeteze mtima wathu,

  Tipewe zoipa.

  Mawu a Yehova M’lungu,

  Atitsogolere.

  Anthu okhulupirika;

  Amawakondadi.

  Choncho timulambiretu

  Monga bwenzi lathu.