Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 34

Kuyenda ndi Mtima Wosagawanika

Sankhani Zoti Mumvetsere
Kuyenda ndi Mtima Wosagawanika
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 26)

 1. 1. Mundiweruzetu Mbuye wanga;

  Onani kuti ndimakudalirani.

  Ndifufuzeni ndi kundiyesa;

  Konzani mtima wanga, mundidalitse.

  (KOLASI)

  Koma ine ndatsimikizadi

  kusonyeza mtima wosagawanika.

 2. 2. Sindikhala ndi anthu oipa.

  Ndimadana ndi onyoza choonadi.

  Chonde musachotse moyo wanga

  Ndi anthu oipa okonda ziphuphu.

  (KOLASI)

  Koma ine ndatsimikizadi

  kusonyeza mtima wosagawanika.

 3. 3. Ndikonda kukhala m’nyumba yanu.

  Ndimasangalala kukulambirani.

  Ndidzayendadi kuguwa lanu,

  Pokuyamikani mokweza kwambiri.

  (KOLASI)

  Koma ine ndatsimikizadi

  kusonyeza mtima wosagawanika.

(Onaninso Sal. 25:2.)