Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 31

Yendani ndi Mulungu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Yendani ndi Mulungu
ONANI

(Mika 6:8)

 1. 1. Yendanitu ndi Mulungu;

  Musonyeze chikondi.

  Ndipo musachoke kwa Yehova,

  Akulimbitsenitu.

  Mawu akewo muzisunga;

  Simudzasochera.

  Muzimveratu Mulungu

  Akutsogolereni.

 2. 2. Yendanitu mu chiyero;

  Muzipewa zoipa.

  Mayesero angakule bwanji,

  Mudzawapiliratu.

  Zinthu zonse zotamandika

  Ndiponso zoona,

  N’zomwe muziganizira,

  M’lungu sakusiyani.

 3. 3. Yendanitu ndi Mulungu;

  Mudzasangalaladi.

  Zabwino zomwe amapereka

  Muzimuthokozatu.

  Yendanibe ndi M’lungu wathu;

  Muzimuimbira.

  Chimwemwecho ndi umboni,

  Woti ndinu a M’lungu.