Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 27

Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera

Sankhani Zoti Mumvetsere
Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Aroma 8:19)

 1. 1. Posachedwa M’lungu wathu

  Odzozedwa ake,

  Adzawasonyeza kuti

  ndi ana akedi.

  (KOLASI)

  Khristu ndi odzozedwawo

  Adzapambanadi.

  Ulemerero wawonso

  Udzaonekera.

 2. 2. Posachedwa otsalira

  Adzaitanidwa.

  Khristu Mfumu ya mafumu,

  adzatenga onse.

  (KOLASI)

  Khristu ndi odzozedwawo

  Adzapambanadi.

  Ulemerero wawonso

  Udzaonekera.

  (VESI LOKOMETSERA)

  Limodzi ndi Mbuye wawo

  adzamenya nkhondo.

  Ukwati ndi Mbuye Yesu

  Udzachitikatu.

  (KOLASI)

  Khristu ndi odzozedwawo

  Adzapambanadi.

  Ulemerero wawonso

  Udzaonekera.