ONANI

(Mateyu 25:34-40)

 1. 1. Nkhosa zina zomwe Yesu ali nazo,

  zimatumikira ndi odzozedwa.

  Zomwe nkhosa zina

  zingawachitire

  Yesu adzawabwezeratu zonse.

  (KOLASI)

  “Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.

  Zonse zimene munawachitira

  munachitiranso ine amene.

  Zonse zomwe munawachitira.

  Munachitiranso ine amene.”

 2. 2. “Pamene ndinali wanjala, waludzu,

  munandithandiza mwamsanga ndithu.”

  “Mbuye, tinachita

  liti zimenezi?”

  Ndiyeno Mfumu idzayankha kuti:

  (KOLASI)

  “Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.

  Zonse zimene munawachitira

  munachitiranso ine amene.

  Zonse zomwe munawachitira.

  Munachitiranso ine amene.”

 3. 3. “Mwakhulupirika pochita zabwino,

  polalikira ndi abale anga.”

  Choncho Mfumuyo

  idzauza nkhosazo:

  “Landirani dziko, moyo wangwiro.”

  (KOLASI)

  “Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.

  Zonse zimene munawachitira

  munachitiranso ine amene.

  Zonse zomwe munawachitira.

  Munachitiranso ine amene.”