NYIMBO 23
Yehova Wayamba Kulamulira
1. Ufumu wa Mulungu.
Wayamba kulamula.
Khristu ndiye mwala mu Ziyoni.
Tonse tikweze mawu.
Tiimbire Mulungu.
Khristu Mpulumutsi,
wakhala pampando.
(KOLASI)
Ufumu ubweretsa chani?
Choonadi n’chilungamo.
Udzabweretsanso chiyani?
Moyo wosatha n’chimwemwe.
Tamanda Mfumu yosatha
Iye ndi wachikondi.
2. Khristu ali pampando,
Amagedo yafika.
Dongosolo la Satana litha.
Choncho tilalikire.
Ambiri amve mawu;
Ofatsa onse abwere
kwa Mulungu.
(KOLASI)
Ufumu ubweretsa chani?
Choonadi n’chilungamo.
Udzabweretsanso chiyani?
Moyo wosatha n’chimwemwe.
Tamanda Mfumu yosatha
Iye ndi wachikondi.
3. Tilemekeza Mfumu.
Yomwe ndi yodabwitsa.
Ikubwera m’dzina la Mulungu.
Lowani pachipata;
M’lungu mum’pembedzere.
Posachedwa
adzalamulira dziko.
(KOLASI)
Ufumu ubweretsa chani?
Choonadi n’chilungamo.
Udzabweretsanso chiyani?
Moyo wosatha n’chimwemwe.
Tamanda Mfumu yosatha
Iye ndi wachikondi.
(Onaninso 2 Sam. 7:22; Dan. 2:44; Chiv. 7:15.)