Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

MITU YA NKHANI

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 19

Chakudya Chamadzulo cha Ambuye

Sankhani Zoti Mumvetsere
Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 26:26-30)

 1. 1. Yehova ’Tate wakumwamba,

  Usikuwu n’ngwapadera.

  Kale patsikuli munasonyezatu

  Chikondi, nzeru ndi mphamvu.

  Mwana wankhosa anaphedwa,

  Anthu anamasulidwa.

  Kenako Yesu anakhetsa magazi

  Kukwaniritsa ulosiwu.

 2. 2. Mkate ndi vinyo n’zokumbutsa,

  Kufunika kwa nsembeyi.

  Komanso mphatso

  yomwe munatipatsa,

  Mwana wanu wokondedwa.

  Madzulo ano tiyenera,

  Kuchita chikumbutsochi

  Pokumbukira

  zomwe zinachitika

  Kuti dipo liperekedwe.

 3.  3. Tasonkhana pamaso panu.

  Tamva kuitana kwanu

  Titamande inu

  ndi Mwana wanunso

  Munatikonda kwambiri.

  Mwambo wokulemekezani

  Umatilimbikitsanso.

  Tiyendebe motsatira Yesu Khristu,

  Ndipo tidzapezadi moyo.