ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Chivumbulutso 21:2)

 1. 1. Yehova ’nadzoza Yesu

  Kuti alamulire.

  Kuti chifuniro cha M’lungu,

  Padzikoli chichitike.

  (KOLASI)

  Tamandani Yehova M’lungu,

  Chifukwa cha wodzozedwa.

  Inu nkhosa zokhulupirika

  Zomvera malamulo.

  Tamandani wodzozedwayo,

  Wolamula wakumwamba,

  Amene adzayeretsa dzina

  Loyera la Mulungu.

 2. 2. Abale a Yesu Khristu.

  M’lungu amawasankha.

  Adzalamulira ndi Yesu

  Dzikoli adzayeretsa.

  (KOLASI)

  Tamandani Yehova M’lungu,

  Chifukwa cha wodzozedwa.

  Inu nkhosa zokhulupirika

  Zomvera malamulo.

  Tamandani wodzozedwayo,

  Wolamula wakumwamba,

  Amene adzayeretsa dzina

  Loyera la Mulungu.