ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Aheberi 1:6)

 1. 1. Tamandani Yesu,

  Mfumu yodzozedwayo.

  Yokonda choonadi;

  Komanso chilungamo.

  Popereka ulemu

  Ku dzina la M’lungu,

  Ulamuliro wake,

  Adzalengezatu.

  (KOLASI)

  Tamandani Yesu!

  Wodzozedwa wa M’lungu.

  Wakhala pa Ziyoni,

  Mongatu Mfumu yathu!

 2. 2. Tamandani Yesu,

  Yemwe anatifera.

  Anapereka dipo;

  Timakhululukidwa.

  Mkwatibwi wake pano

  Akudikirira.

  Ukwati n’ngwakumwamba

  Udzakweza M’lungu.

  (KOLASI)

  Tamandani Yesu!

  Wodzozedwa wa M’lungu.

  Wakhala pa Ziyoni,

  Mongatu Mfumu yathu!