ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Ekisodo 15:1)

 1. 1. Timuimbire Yehova M’lungu wokwezeka.

  Waponyera m’nyanja Aigup’to onyada.

  Titamande Ya;

  Palibenso Mulungu wina.

  Yehova ndi dzina lake;

  ndi wopambana.

  (KOLASI)

  Yehova ndinu wokwezeka,

  Simunasinthe ndinudi Mfumu,

  Posachedwa ’dani mugonjetsa

  N’kuyeretsa dzina lanu.

 2. 2. Mitundu yonse ikutsutsana ndi Yehova.

  Ichita manyazi,

  Ngakhale ndi yamphamvu.

  Pachiweruzo;

  Singathawetu Amagedo.

  Idzadziwa kuti

  Yehova ndi Mulungu.

  (KOLASI)

  Yehova ndinu wokwezeka,

  Simunasinthe ndinudi Mfumu,

  Posachedwa ’dani mugonjetsa

  N’kuyeretsa dzina lanu.