ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 37:29)

 1. 1. Mulungu watilonjeza.

  Moyo womwe sudzatha.

  ‘Ofatsa ’dzasangalala.’

  Zidzachitikadi.

  (KOLASI)

  Tidzakhala ndithu,

  Ndi moyo wosatha.

  M’lungu walonjeza.

  Zidzachitika.

 2. 2. Paradaiso akubwera;

  Anthu adzamasuka.

  Kudzakhaladi mtendere,

  Wochoka kwa M’lungu.

  (KOLASI)

  Tidzakhala ndithu,

  Ndi moyo wosatha.

  M’lungu walonjeza.

  Zidzachitika.

 3. 3. Akufawo adzauka,

  Chisoninso chidzatha.

  Mulungu adzapukuta,

  Misozi ya anthu.

  (KOLASI)

  Tidzakhala ndithu,

  Ndi moyo wosatha.

  M’lungu walonjeza.

  Zidzachitika.