Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 146

“Ndikupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano”

Sankhani Zoti Mumvetsere
“Ndikupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano”
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Chivumbulutso 21:1-5)

 1. 1. “Zizindikiro” zikusonyezatu.

  Kuti Yesu akulamulira.

  Wachotsatu Satana kumwamba,

  Posachedwa am’chotsa padziko.

  (KOLASI)

  Sangalalani chifukwa,

  M’lungu alitu ndi anthu.

  Iye adzachotsatu imfayi,

  Chisoni ndiponso zowawazi.

  ‘Zonse zidzakhala zatsopano.’

  Mawuwa ndi oona.

 2. 2. Anthu aone Yerusalemuyo,

  Mkwatibwi wa Mwana wa Nkhosayo,

  Atavala mochititsa chidwi,

  Yehova ndiye kuwala kwake.

  (KOLASI)

  Sangalalani chifukwa,

  M’lungu alitu ndi anthu.

  Iye adzachotsatu imfayi,

  Chisoni ndiponso zowawazi.

  ‘Zonse zidzakhala zatsopano.’

  Mawuwa ndi oona.

 3. 3. Mzindawu udzasangalatsa anthu.

  Uzidzakhala wosatsekedwa.

  Anthu adzayendatu mowala;

  Atumikinu muziwalabe.

  (KOLASI)

  Sangalalani chifukwa,

  M’lungu alitu ndi anthu.

  Iye adzachotsatu imfayi,

  Chisoni ndiponso zowawazi.

  ‘Zonse zidzakhala zatsopano.’

  Mawuwa ndi oona.