ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(2 Akorinto 4:18)

 1. 1. Pomwe osaona ’kuwona

  Ovutika kumva akumva,

  Ana adzaimbanso nyimbo,

  Mtendere padziko lonse,

  Omwe anafa adzauka,

  Uchimo, mavuto zathanso,

  (KOLASI)

  Mudzaona zinthu zonsezi,

  M’kayang’anabe pamphoto.

 2. 2. Mimbulu idzadya ndi nkhosa,

  Zilombo zoopsa ndi ng’ombe,

  Mwana adzazitsogolera,

  Zidzamvera mawu ake.

  Pamene misozi idzatha,

  Mantha ndi zowawa zathanso,

  (KOLASI)

  Mudzaona zinthu zonsezi,

  M’kayang’anabe pamphoto.