Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 141

Moyo Ndi Wodabwitsa

Sankhani Zoti Mumvetsere
Moyo Ndi Wodabwitsa
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 36:9)

 1. 1. Makanda onse, ndiponso mvula,

  Mbewu komanso kuwala kwa dzuwa​—

  Mulungu ndiye amatipatsa

  mphatsozi ndipo zimatithandizadi.

  (KOLASI)

  Tingachite chani ndi mphatso iyi?

  Tikonde Mulungu yemwe anatipatsa.

  Sitingaipeze mphatsoyi patokha,

  Mphatso yake ndiyo moyo wodabwitsa.

 2. 2. Ena ’ngasiye kulimba mtima,

  N’kunena kuti: ‘Kuli bwino kufa.’

  Koma ifeyo sitili choncho.

  Timayamikira kukhala ndi moyo.

  (KOLASI)

  Tingachite chani ndi mphatso iyi?

  Tikonde anzathu amene tili nawo.

  Sitingaipeze mphatsoyi patokha,

  Mphatso yake ndiyo moyo wodabwitsa.