ONANI

(Salimo 2:12)

 1. 1. Khamu lochokera m’mitundu

  yonse lasonkhana,

  Khristu ndi odzozedwa

  akulisonkhanitsatu.

  Ufumu wa Mulungu wabadwa;

  Tipempha ubwere.

  Chiyembekezochi ndi mphatso,

  Chimatisangalatsadi.

  (KOLASI)

  Tamandani M’lungu; Tamandani Yesu​—

  Iye ndi Mfumu ya mafumu.

  Mogwirizana timvera Yesu

  Ndiponso tim’tamanda.

 2. 2. Titamande Mfumu yathu poimba,

  mwachimwemwe.

  Kalonga Wamtendereyu

  adzatipulumutsa.

  Tidzasangalala kukhala

  M’dziko mopanda mantha,

  Akufa adzawaukitsa.

  Tonse tidzasangalala.

  (KOLASI)

  Tamandani M’lungu; Tamandani Yesu​—

  Iye ndi Mfumu ya mafumu.

  Mogwirizana timvera Yesu

  Ndiponso tim’tamanda.