ONANI

(Miyambo 16:31)

 1. 1. Pano tili ndi anthu

  Achikulire.

  Akukondabe M’lungu;

  Sanamusiye.

  Enatu umasiye

  Ukuwawawa

  Tate, atonthozeni,

  Alimbitseni.

  (KOLASI)

  Mumakumbukira

  Zochita zawo.

  Tate auzeni:

  “Mwachita bwino!”

 2. 2. Imvi za olungama

  Ndi zokongola.

  Zimasangalatsadi

  Tate Yehova.

  Ife tikumbukire

  Pa nthawi ina.

  Pa unyamata wawo

  Ankayesetsa.

  (KOLASI)

  Mumakumbukira

  Zochita zawo.

  Tate auzeni:

  “Mwachita bwino!”