Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 136

Yehova “Akufupe Mokwanira”

Sankhani Zoti Mumvetsere
Yehova “Akufupe Mokwanira”
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Rute 2:12)

 1. 1. Yehova amadziwa anthu onse

  Omwe amam’tumikira.

  Amadziwa bwino mavuto awo,

  Zomwe amadzimananso.

  Ngati mwasiya abale ndi nyumba,

  Zonse M’lungu akudziwa.

  Amatipatsa ’bale auzimu,

  Moyo m’dziko latsopano.

  (KOLASI)

  Yehova akupatseni mphoto.

  Akufupeninso mokwanira.

  Mubisale m’mapiko ake.

  N’ngokhulupirika, sanganametu.

 2. 2. Nthawi zina timakhala ndi nkhawa

  Poganizira moyowu.

  Mwinanso kupeza zofunikira

  Kungakhaletu kovuta.

  M’lungu amadziwa zomwe m’mafuna,

  Amamvanso mapemphero.

  Mawu, mzimu wake ndi mabwenzinso

  Adzakulimbikitsani.

  (KOLASI)

  Yehova akupatseni mphoto.

  Akufupeninso mokwanira.

  Mubisale m’mapiko ake.

  N’ngokhulupirika, sanganametu.