ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mlaliki 12:1)

 1. 1. Anyamata ndi atsikanafe,

  Ndife ofunika kwa Mulungu.

  Tikamam’tumikira mwakhama,

  Azitidalitsa nthawi zonse.

 2. 2. Tikamalemekeza makolo

  Timawasonyezatu chikondi.

  Anthu ndi M’lungu amatikonda,

  Tidzayandikira M’lungu wathu.

 3. 3. Tizikumbukira M’lungu wathu,

  Tizikonda cho’nadi kwambiri.

  Tikakhulupirika kwa M’lungu,

  Tidzasangalatsadi Yehova.