ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Genesis 2:23, 24)

 1. 1. Fupa la mafupa anga,

  Ndiwe mnofu wa mnofu wanga.

  M’lungu wandipatsa mnzanga,

  Iwe ndi wangadi.

  Ndife thupi limodzidi;

  Madalitso tizilandira.

  Monga mwamuna ndi mkazi,

  Pano ndife banja.

  Titumikire M’lungu wathu.

  Tsiku ndi tsiku,

  Chikondi tikulitse.

  Zimene talumbirazi.

  Tizichita kwa moyo wonse.

  Tizilemekeza M’lungu,

  Ndipo ukhalebe wanga.