Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 13

Khristu Ndi Chitsanzo Chathu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Khristu Ndi Chitsanzo Chathu
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(1 Petulo 2:21)

 1. 1. Yehova Mulungu,

  Anatikondadi,

  Potipatsa dipo la Mwana wake.

  Khristu anakhala​—

  Ngati anthu tonse​—

  Ndipo analemekeza M’lungu.

 2. 2. Mawu a Yehova,

  Anati n’chakudya.

  Chimene chinamupatsadi nzeru.

  Anatumikira,

  Mofunitsitsadi;

  Ndipo anasangalatsa M’lungu.

 3. 3. Titsanzire Yesu

  Potamanda M’lungu,

  Komanso muzochita zathu zonse.

  M’moyo wathu wonse

  Titsanzire Yesu,

  Ndipo tidzasangalatsa M’lungu.