Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 129

Tipitirizabe Kupirira

Sankhani Zoti Mumvetsere
Tipitirizabe Kupirira
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 24:13)

 1. 1. Tiyenera

  Kumapirira mayesero.

  Paja Yesu

  Anachitanso zimenezo.

  Analimba mtima,

  Podalira M’lungu.

  (KOLASI)

  Tikhale opirira

  tizilalikira.

  M’lungu amatikonda.

  Adzatithandiza kupirira.

 2. 2. Tingakumane

  Ndi mavuto ochuluka,

  Komabe moyo

  wosatha tidikirira.

  Mtendere wosatha

  tikulakalaka.

  (KOLASI)

  Tikhale opirira

  tizilalikira.

  M’lungu amatikonda.

  Adzatithandiza kupirira.

 3.  3. Sitichita

  mantha kapena kukayika.

  Titumikire

  Mpaka tsiku lomaliza.

  Tsiku la Yehova

  lilidi pafupi.

  (KOLASI)

  Tikhale opirira

  tizilalikira.

  M’lungu amatikonda.

  Adzatithandiza kupirira.