Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 128

Tipirire Mpaka Mapeto

Sankhani Zoti Mumvetsere
Tipirire Mpaka Mapeto
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 24:13)

 1. 1. Mawu a Mulungu wathu

  Amalimbikitsa.

  Zonse zomwe waphunzira

  N’zolondola, n’zoona.

  Limba m’chikhulupiriro,

  Tsiku la Ya lafika.

  Usaope mayesero;

  Udzakhala wolimba.

 2. 2. Chikondi chako kwa M’lungu,

  Chisachepe mphamvu.

  Upirirebe ngakhale,

  Mayesero akule.

  Kaya akhale otani,

  Usachitetu mantha.

  Yehova Mulungu wako,

  Adzakupulumutsa.

 3.  3. Yemwe angapirirebe

  Adzapulumuka.

  M’buku la moyo la M’lungu,

  Adzalembedwamotu.

  Lola kuti kupirira;

  Kugwire ntchito yake.

  Yehova adzachititsa;

  Kuti usangalale.