Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 122

Khalani Olimba Komanso Osasunthika

Sankhani Zoti Mumvetsere
Khalani Olimba Komanso Osasunthika
ONANI

(1 Akorinto 15:58)

 1. 1. Mitundu yavutika kwambiri.

  Anthu akuopa zam’tsogolo.

  Ife tilimbe tisasunthike,

  Potumikira M’lungu.

  (KOLASI)

  Tiyenera kulimba;

  Tisiyane ndi dziko,

  Tikhale olimba,

  moyo tidzapeza.

 2. 2. Misampha ndi yambiri m’dzikoli.

  Koma mwanzeru tingaipewe.

  Tikamadana n’zoipa zonse

  Sitidzasunthikadi.

  (KOLASI)

  Tiyenera kulimba;

  Tisiyane ndi dziko,

  Tikhale olimba,

  moyo tidzapeza.

 3. 3. Tizilambira Mulungu wathu.

  Tim’tumikire ndi mtima wonse.

  Tizilalikiradi mwachangu.

  Mapeto akubwera.

  (KOLASI)

  Tiyenera kulimba;

  Tisiyane ndi dziko,

  Tikhale olimba,

  moyo tidzapeza.