Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 120

Tikhale Ofatsa Ngati Khristu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Tikhale Ofatsa Ngati Khristu
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 11:28-30)

 1. 1. Yesu anali wamkulu kwa anthu;

  Koma sanadzikuze, sananyade.

  Anali ndi udindo wapamwamba;

  Komatu anali wodzichepetsa.

 2. 2. Kwa anthu omwe ali ndi mavuto,

  Yesu akuti: ‘Mundisenze onse.’

  Akamafuna Ufumu choyamba.

  Iye adzawachitira chifundo.

 3. 3. Yesu anati, ‘tonse ndi abale.’

  Timamumvera monga Mutu wathu.

  Ofatsa ndi ofunika kwa M’lungu;

  Adzalandira dziko lapansili.